MAFCO IPEREKA CHILANGO KWA OSEWERA OPONDA LUNGU
Timu ya MAFCO yadzudzula khalidwe la osewera ake atatu lomwe anaonetsa pa masewero omwe amasewera ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets pomwe anamuponda mwadala Wongani Lungu mpaka kuvulala.
Timuyi yalemba kalata yopepesa kwa katswiriyu komanso FCB Nyasa Big Bullets kamba ka khalidweli lomwe ladzudzulidwa ndi anthu ochuluka kwambiri mdziko muno.
Iyo yati osewera omwe anachita izi ali mmanja mwawo ndipo Duncan Mwale, Blessings Chandiyang'ana komanso Vitumbiko Phiri apatsidwa chilango ku timuyi kamba kochita khalidwe lonyasa tero.
Pomaliza, timuyi yati imatsatira malamulo omwe bungwe la Super League of Malawi lili nawo ndiponso lipitiliza ubale wawo wabwino ndi matimu onse mdziko muno.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores