"NDI ZAMPIRA TSIKU LINA TIDZAWINA" - KUMWEMBE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya MAFCO, Macdonald Kumwembe, wati wavomereza kuti masewero anawavuta ndipo kwa lero sanapambane koma alimbikira kuti tsiku lina adzapambane.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-1 ndi timu ya Karonga United pa bwalo la Rumphi ndipo wati akonza mavuto awo mmasewero omwe akudzawa.
"Ndi zampira basi zimachitika mu mpira kuti timu imagonja ena amapambana nde lero zakomera anzathuwa tiwayamikire Ife zativuta tidzapambananso mmasewero ena." Anatero Kumwembe.
Iye wati timu yake inayesetsa kulimbikira kuti mwina ipezeko chigoli chachiwiri atagoletsa chobwenzera koma kuchita zinthu mogona kwachititsa kupezetsa zigoli ziwiri mmasewerowa.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachikhumi (10) pomwe ili ndi mapointsi okwana 27 pa masewero 21 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores