NDIME YOTSIRIZA YA FDH BANK ILIKO SABATA YA MAWA
Bungwe la Football Association of Malawi latsimikiza kuti masewero amu ndime yotsiriza ya chikho cha FDH Bank adzaseweredwa lamulungu pa 01 September 2024.
Bungweli watsimikiza za nkhaniyi kudzera pa tsamba lawo lamchezo kuti bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe ndi limene lichititse masewerowa.
Matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Blue Eagles akuyembekezeka kudzakumana mmasewerowa kutsatira matimu onse kufika mu ndimeyi.
Timu ya Blue Eagles inagonjetsa Karonga 2-0 kuti ifike mu ndimeyi ndipo yatulutsapo matimu ngati a Silver Strikers ndi Baka City pomwe Bullets inaswa Moyale Barracks 3-1 ndipo yatulutsaponso matimu ngati a Mighty Mukuru Wanderers komanso Civil Service United.
Wolemba: Hastings Kasonga
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores