"TIKUFUNA KUTHERA KU MATIMU ANAYI OYAMBA" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Oscar Kaunda, wati timu yake ikuyang'ana zothera ku matimu anayi oyambilira mu ligi pomwe wati mchigawo chachiwiri alimbikira kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 1-1 ndi timu ya Mzuzu City Hammers lachitatu pa bwalo la Karonga ndipo wati masewero anali ovuta kwambiri poti maseweredwe akufanana ndi Hammers.
Iye wati timu yake ikufunitsitsa kuti izichita bwino kuti ichoke kumunsi kumene ili ndipo kuti awonjezera osewera poti alipo ochepa.
"Inde tiwonjezera kaya asanu poti tili ndi osewera ochepa kwambiri kaya 20 pomwe 17 ankati ndipo atatu apagolo nde masewerowa ndi ochuluka sizikugwira. Tikuyang'ana zothera ku matimu anayi oyamba mu ligi ndipo tikanilitsadi chifukwa ndi omwe ali kuchokera pachitatu sitikutaya kwambiri." Anatero Kaunda.
Karonga ili ndi mapointsi okwana 19 pa masewero 15 omwe yasewera ndipo ikadali pa nambala 11.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores