Timu ya Ascent Academy yaikidwa mu Gulu B yampikisano wa COSAFA CAF Women's Champions League Qualifiers malingana ndi mayere omwe bungwe la COSAFA inachita lachitatu masana.
Timuyi idzakumana ndi timu ya Gaborone United Ladies yaku Botswana, Uniao Desportivo de Lichinga yaku Mozambique komanso Young Buffaloes yaku Eswatini.
Mu gulu A la mpikisanowu muli University of Western Cape FC yaku South Africa, Green Buffaloes yaku Zambia, Herental Queens yaku Zimbabwe komanso FC Ongos Ladies yaku Namibia.
Mpikisanowu uchitika ku Malawi mu mzinda wa Blantyre kuyambira mwezi wa mawa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores