"MASEWERO ONSE TASEWERA BWINO" - MZUNGA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya MAFCO, Jimmy Mzunga, wati timu yake inasewera bwino kwambiri mmasewero awo ndi timu ya Karonga United zomwe zawathandizira kuti achite bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 2-0 pa bwalo la Chitowe ndipo wati akufunitsitsa kuti azichita bwino pa masewero awo onse omwe azisewera mu ligi.
"Masewero abwino kwambiri tasewera bwino mchigawo choyamba komanso chachiwiri nde zatithandiza kuti tichite bwino nde ndife osangalala kwambiri." Anatero Mzunga.
Timuyi tsopano yafika pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe ili ndi mapointsi 19 pa masewero 13 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores