"POKUTHA PA LERO TIBWERA PA 2" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati timu yake isuntha kuchoka pa nambala yachisanu kufikira pa nambala yachiwiri akamatha masewero awo ndi Civil Service United poti iwo achita bwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe pa bwalo la Civo masana a lachitatu ndipo iye wati akonzekera bwino ndipo chipambano ndi Bangwe chiwalimbikitse kuti apambane leronso.
"Takonzekera bwino masewerowa tikudziwa tonse timagwiritsa ntchito bwalo limodzi komabe mpira ndi pa bwalo la zamasewero nde tawauza anyamata kufunikira kwa ma pointsi amenewa nde pakutha pa masewerowa tisuntha tifika pa 2", anatero Mtetemera.
Iye watinso alibe wosewera aliyense wovulala mu timuyi ndipo chomwe akupitira ndi chipambano chokha basi.
Timu ya Creck ili pa nambala yachisanu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 19 pa masewero 12 omwe yasewera mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores