"TINAFOOKA MCHIGAWO CHACHIWIRI" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati timu yake yagonja masewero ake ndi FCB Nyasa Big Bullets kamba koti mchigawo chachiwiri anafooka.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 5-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati iwo anatsegula mmbali mwa timuyi mpake anachinyitsa zigoli zisanu mchigawo chachiwiri.
"Zimene zinativuta ndi zoti timakanika kuchinya mchigawo choyamba tinachilimika koma mchigawo chachiwiri tinafooka kwambiri. Tinatsegula mmbali zomwe zinatichititsa kuti tichinyitse kwambiri." Anatero Yasin.
Zateremu, timuyi tsopano yatuluka mu chikho cha FDH Bank ndipo timu ya Bullets yapitilira mu mpikisanowu kufika mu ndime ya matimu khumi, asanu ndi mmodzi (16).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores