"TIKAYESETSABE KUTI TIKACHITE BWINO" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati timu yake ikuyembekezera masewero ovuta kwambiri pomwe akukumana ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets koma wati akayesetsa kuti akachite bwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe lamulungu pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yake sikuopa poti masewero amu chikho amatha kukomera timu iliyonse.
"Ndi masewero ovuta kwambiri poti Bullets ndi timu yaikulu komanso ikutetezs chikho chimenechi nde si ntchito yophweka kuti achitaye komabe takonzeka bwino kuti tikayesetse kuchita bwino mmasewerowa." Anatero Yasin.
Timu ya Bangwe All Stars ikuchokera kosachita bwino mu ligi ya TNM pomwe inagonja 2-0 ndi Baka City ndipo yagonja masewero onse omwe yakumanako ndi Bullets mu chaka chatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores