SULOM IYIKA MASEWERO A MKATI MWA SABATA
Bungwe loyendetsa mpira wamu ligi yaikulu mdziko muno la Super League of Malawi lati kutuluka kwa ndandanda wosintha wa masewero amu ligiyi utuluka pa 18 June 2024 osati lero ngati mmene ananenera.
Bungweli latsimikiza za nkhaniyi lachisanu kudzera pa website yawo ndipo lati kusinthaku kwadza kamba ka imfa ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Saulos Klaus Chilima komanso anthu ena asanu ndi atatu ndi kulengeza kolira malirowa kwa masiku 21.
Bungweli lati kusintha Kwa masewerowa kwaunikiranso dandaulo la matimu kuti aziseweranso mkati mwa sabata ndi cholinga choti asokerere ndi pomwe paphonyedwa kale malingana ndi chikonzero chapoyamba.
Kusintha pa ndandanda umenewu kwadza pomwe matimu angapo anadandaula ndi mmene masewero akuyendera pomwe ena amayenda kwambiri koma ena amasewera kwambiri pakhomo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores