"NDE CHOKHALIRA NDI OYIMBIRA NDI CHANI?" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO, Gilbert Chirwa, wati timu yake yagonja kamba koti oyimbira amawakondera anyamata a Creck Sporting Club ndipo sanayimbire bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa bwalo la Civo ndipo wati timu ya Creck inayamba kuchedwetsa mpira mu chigawo choyamba chomwe koma oyimbira samachita kalikonse.
"Analidi masewero a msinkhu wathu koma masewerowa avuta chifukwa cha anzathu oyimbira. Creck inayamba kuchedwetsa mpira mchigawo choyamba, achinya chigoli chabwino koma kungotero nde oyimbira osawaletsa komanso kumangotiyimbira chilichonse nde zinawapatsa mphamvu a Creck ndikufooketsa anyamata athu." Anatero Chirwa.
Iwe wati timu yake yaonetsa kuti ili tsopano bwino ndipo anangovutika poti anaphonya mipata yochuluka mchigawo choyamba.
FOMO ili pa nambala 12 pomwe ili ndi mapointsi 7 pa masewero asanu ndi awiri (7).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores