"NDAKHUTITSIDWA NDI POINT IMODZI" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati wakhutira ndi kutenga point imodzi chabe kutengera ndi kuvuta kwa masewero komanso poti akuchoka kogonja ndi Mzuzu City Hammers sabata yatha.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi Moyale Barracks ndipo wati akukhulupilira kuti masewero alinkudza akhale akupeza chipambano.
"Anali masewero ovuta kwambiri chifukwa anzathuwa anabwera movuta kwambiri ifenso tinali bwino koma mipata yomwe tinapeza tinaphonya nde tikuchokera kogonja apa tafanana mphamvu ndekuti sabata inayi tidzapambana koma point imodzi ndakhutira." Anatero Kamanga.
Iye wati akhale akukonza mavuto awo omwe awaona mmasewerowa ndipo sabata ya mawa adzachita bwino.
Timuyi ikadali pa nambala yachisanu (5) mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 12 pa masewero 7 yomwe yasewera pomwe yapambana katatu, kufanana mphamvu katatu ndi kugonja kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores