SAPOTA WA FOMO WAMENYEDWA PA CIVO
Wachiwiri wa wapampando wa komiti ya ochemelera a timu ya FOMO mchigawo chapakati, Peter Malata ali ku chipatala komwe akulandira thandizo atamenyedwa ndi anthu omwe akuganiziridwa kuti ndi masapota atimu ya Clerk Sporting club.
Malingana ndi mlembi wamkulu wa komiti ya masapota FOMO mchigawochi, Felix Gunya, wati anthuwa anafika pa bwalo la CIVO kuzachita za zikhulupiliro zawo pamapeto a zokonzekera za timu ya FOMO, ndipo pokanizidwa kulowa mu bwaloli anayamba kumenya wachitetezo wa FOMO pamodzi ndi wapampandoyi.
Iye wati mwamwayi, wachitetezo anapeza mpata othawa ndipo tsopano ali ku chipatala.
Matimu a Creck Sporting Club komanso FOMO akumane pa masewero awo mu TNM Supa ligi pa bwalo la Civo pa nkhondo yotolera mapointsi.
Source: FOMO FC
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores