"TIKUKAPAMBANA MWA NJIRA ILIYONSE" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati timu yake ikhale ikupeza chipambano mwa njira iliyonse pomwe akhale akusewera pakhomo loweruka.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe asewere ndi Chitipa United pa bwalo la Dedza ndipo wati zokonzekera zawo zayenda bwino ndipo chatsala ndi kupeza chipambano basi.
"Zokonzekera zayenda bwino kwambiri ndipo anyamata akuoneka bwino kutengera ndi mmene akuthamangira komanso ku mbali ya ovulala nde tili okondwa ndi mmene tilili ndipo mwa njira iliyonse mawa tipeza chipambano." Anatero Bunya.
Iye anati akudalira osewera aliyense poti onse ali mu dongosolo lake ndipo malingana ndi mpikisano pakati pa anyamatawo akumasowa kuti ayambitsa ndani.
Timu ya Dedza ili pa nambala yachikhumi (10) pomwe yatolera mapointsi asanu ndi awiri (7) pa masewero asanu ndi amodzi (6) omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores