"TAKONZA NDI PA BENCH POMWE" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Nginde Mtetemera, wati timu yake tsopano yakonza mavuto awo onse omwe amakumana nawo mmasewero omwe akhala asakuchita bwino ndipo akukhulupilira kuti achita bwino loweruka.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe asewere ndi timu ya FOMO pa bwalo la Civo ndipo wati akonzeka kuti akapambanepo pa masewerowa.
"Takonza monse pagolo, kumbuyo, pakati komanso kutsogolo, angakhale pa bench ndi malo nde takonzekera ndithu kuti tikatenge chipambano, tikuyenda tsopano bwino chifukwa tsopano timuyi ikukonzeka bwinobwino." Anatero Mtetemera.
Iye wati yakwana nthawi tsopano kuti awapepese masapota atimuyi ndi chipambano ndipo tsopano mwa njira iliyonse Iwo apambana.
Timu ya Creck Sporting Club ili pa nambala 11 pomwe yapambana masewero awiri, kufanana mphamvu kamodzi ndi kugonjanso katatu ndipo ali ndi mapointsi asanu ndi awiri (7).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores