"ANYAMATA ASEWERA BWINO KWAMBIRI" - MWASE
Wothandizira mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wayamikira osewera ake kamba kusewera mpira mwapamwamba zomwe zachititsa kuti apambane masewero awo loweruka.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 3-0 ndi Creck Sporting Club ndipo wati anyamata ake anachotsa mantha pa timuyi kuti apambane mmasewerowa.
"Tiwathokoze osewera athu kamba kosewera mwapamwamba ndipo tapambana, Creck imaopsa potengera ndi mnene yakhala ikuchitira komabe Ife tinawachotsa mantha, amenya mpira womwe amadziwa ndipo zoonadi tapambana." Anatero Mwase.
Mphunzitsiyu anadandaulako za kuphonya mipata yochuluka mmasewerowa koma wati akonza mavutowa kupita chitsogolo.
Timuyi ili pamwamba pa ligi pomwe yatolera mapointsi asanu ndi awiri (7) pa masewero atatu omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores