"BAKA CITY ILI NDI TSOGOLO LABWINO" - MUYOMBE
Mphunzitsi watimu ya Baka City, Davie Muyombe, wati timu yake ikhale ikuchita bwino muligi ya TNM mmasewero akutsogoloku kamba koti akadaphunzira mmene mpira wamu ligiyi umayendera.
Iye amayankhula atagonja 2-1 ndi timu ya Mzuzu City Hammers kuti akhale masewero awiri opanda chipambano ndipo wati timu yake ndi yabwinobwino komanso ili ndi tsogolo labwino.
"Palibe mavuto aliwonse timu ilibwinobwino kungoti mwina poti tikumenya ligi yaikulu koma tiphunzira mmene mpira wake umayendera nde tikasewera masewero asanu kapena kudutsa apo tidzachita bwino kwambiri." Anatero Muyombe.
Iye anatinso masewerowa akanakhala ophweka kuti apambane koma ziganizo zina za oyimbira sizinali zabwino mmasewerowa.
Timuyi ili pa nambala 15 pomwe ilibe point iliyonse pa masewero awiri amene Iwo asewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores