"TINAYICHENJERERA DEDZA KUTI TICHITE BWINO" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wati chigoli cha msanga chinawathandiza kuti achite bwino ndipo ndi wokondwa kamba kopambana.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 3-0 ndi Dedza Dynamos ndi zigoli za Kelvin Kadzinje, Muhammad Biason komanso Emmanuel Savieli ndipo wati awalimbikitse osewera ake kuti azichitabe bwino.
"Anali masewero ovuta koma tinawachenjerera anzathuwa pomwe chigoli cha msanga chinatithandiza kwambiri kuwafoola koma tachita bwino, ku Mzuzu sabata yatha tinasewera bwino koma kuphonya nde lero tinawalimbikitsa, inde taphonya koma chipambano timachifuna Kwambiri." Anatero Makawa.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachiwiri mu ligi ya TNM pomwe yatolera mapointsi atatu pa masewero awiri omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores