FOMO YAPEZA CHIPAMBANO CHOYAMBA
Timu ya FOMO yapeza chipambano chake choyamba mu ligi ya TNM pomwe yagonjetsa timu ya Bangwe All Stars 1-0 pa bwalo la Mulanje masana a loweruka.
Hassan Luwembe anamwetsa chigoli pa mphindi 77 za masewerowa kuti timuyi ipambane ndipo mphunzitsi wawo Gilbert Chirwa anati ndi okondwa kamba kopambana masewerowa.
"Ndine wokondwa poti tapambana masewerowa ndipo analidi ovuta koma tinawauza anyamatawa kuti alimbikire mpaka anapeza chigoli, Pali ma dera omwe sitinachite bwino koma tikonza mavutowa kuti kupita chitsogolo tipitilire kuchita bwino." Anatero Chirwa.
Timuyi yalowa kumene mu ligiyi ndipo yapanga mbiri popambana masewero awo enieni oyamba mu ligiyi. Timuyi ili pa nambala yachitatu mu ligi ndi mapointsi atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores