"CHITIPA SI TIMU YOIPA KWAMBIRI" - KAFOTEKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Elvis Kafoteka, wati timu yake yasewera bwino kwambiri ndipo yaonetsa kuthekera kochitanso bwino mu ligi ya 2024.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi Silver Strikers pa bwalo la Silver ndipo wati wakhutira ndi mmene osewerawa anachitira ndi Silver.
"Anali masewero oti tonse timafanana kwambiri mu mphindi 15 zoyambilira komwe sitimawapatsa ulemu a Silver Strikers koma kenako tinayamba kuwawopa nde tinatsegula mipata yonse mpaka anagoletsa komabe asewera bwino kwambiri." Anatero Kafoteka.
Timu ya Chitipa tsopano yapezeka ili pansi penipeni pa ligi pomwe yagoletsetsa zigoli zambiri kuposa timu iliyonse ndipo alibe point iliyonse mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores