"SITINGAYANKHULE ZOTENGA LIGI PANO" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati kuyankhula za kutenga ligi padakali Pano ndi kulawilira kamba koti angosewera masewero amodzi basi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 2-0 ndi Chitipa United ndipo wati anali masewero ovuta koma anyamata ake asewera mwapamwamba.
"Anali masewero ovuta kwambiri makamaka mchigawo choyamba pomwe anzathuwa amamaka pafupi kwambiri koma mchigawo chachiwiri tinasewera bwino tiwayamikire osewera. Sitingayankhule zotenga ligi Pano, inde tikufuna titatenga koma tikutenga masewero aliwonse pa okha kwatsala 29 kutsogoloku." Anatero Mponda.
Timu ya Silver Strikers ili pamwamba pa ligi ya 2024 pomwe ili ndi mapointsi atatu kutsatira kupambanaku.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores