"FOMO SI TIMU YOPHWEKA TIKAVUTIKA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Christopher Nyambose, wachenjeza osewera ake kuti asadelerere timu ya FOMO poti masewero ake akakhala ovuta akakumana pa bwalo la Mulanje loweruka.
Nyambose amayankhula patsogolo pa masewerowa ndipo wati akufunikira kuti achite bwino kuti mzimu wopambana ayende nawo mu ligi ya chaka chino komabe wati masewerowa akhala ovuta.
"Takonzeka kwambiri mmasewerowa ndipo ndili osangalala kuti osewerawa akugwirana mwachangu kwambiri, akale komanso atsopano zomwe zatithandiza kuti tipangeni timu yabwino kwambiri. Tisatengere kuti FOMO tinayichinya ku Betika Four kuja koma iyi ndi ya mapointsi imatha pa mphindi 90 nde tikufunika kuti tisawadelere." Anatero Nyambose.
Timu ya Bangwe ikufunitsitsa kuchita bwino ndi mphunzitsiyu poti chaka Chatha inathera pa nambala yachisanu ndi chimodzi mu ligi ya chaka chatha.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores