"KUSAPAMBANA PA BWALO LA DEDZA SI CHIPHINJO" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa othandizira kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati kusapambana kwawo pa bwalo la Dedza chisakhale chiphinjo watimuyi poti iwo akonzeka kuti akapambanepo.
Munthali amayankhula patsogolo pa masewero omwe akumane ndi Dedza Dynamos mmasewero otsegulira ligi ya 2024 ndipo wati iwo akonzeka kuti akachite bwino mmasewerowa.
"Ndi zoonadi kuti mmasewero omwe tasewera pa bwaloli sitinapambaneko koma sichiphinjo poti Ife masewero aliwonse timawakonzekera mofanana apapa anyamata onse alibwino chimene tikupitira kumeneko ndi chipambano osayang'ana kalikonse." Anatero Munthali.
Iye anatinso anyamata atsopano kutimuyi alibwino koma kwatsala ndi kuwaona kuti angagwirane ndi ndani komanso ngati angachite bwino mmabwalo angati a Dedza ndipo wati Sean McBrams sapezeka kamba koti ndi ovulala.
Bullets ikuyamba chikhochi ngati ochiteteza pomwe akwanitsa kupambana kasanu motsatizana kuchokera mu 2018.
W
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores