"TIKUYENERA KUYAMBA NDI CHIPAMBANO KUTI TIYENDE BWINO" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati timu yake ikuyenera kuyamba ndi chipambano mu ligi ya chaka cha 2024 cholinga choti ulendo wawo wochita bwino uyambe mwapamwamba.
Iye amayankhula patsogolo pokumana ndi timu ya Chitipa United pa bwalo la Silver loweruka ndipo wati kukumana ndi timuyi kukhala kovuta poti imakakamira kwambiri.
"Akhala masewero ovuta kwambiri kutengera kuti Chitipa ndi timu yabwino komanso chaka chatha inathera pa nambala yachinayi sikuti anangogwera koma analimbikira ndithu nde nditimu ya osewera othamanga kwambiri akafuna kukakamira amatha kuchoka ndi point koma takonzeka poti tili pakhomo tikuyenera kupambana kuti ulendo wathu wamu ligi tiyende bwino." Anatero Mponda.
Timu ya Silver ikufunitsitsa itatengako ligi chaka chino pomwe inatenga komaliza mu 2013 ndipo yatenga Mponda kuti awathandizire kupambana chikhochi. Iwo anathera pachiwiri chaka chatha.
Wolemba: Hastings Wadza Ka
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores