"MASEWEROWA AKUTIPATSA CHITHUNZITHUNZI CHABWINO" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda wati masewero omwe akusewera akupereka chithunzithunzi chabwino pa mphamvu za osewera omwe atagwilitse ntchito chaka chino.
Mponda amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Bangwe All Stars 3-0 pa bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji ndipo wayamikira osewera poti akutsatira zomwe akuwauza.
"Masewero akupatsa mwayi oti tidziwe kuti ndi osewera ati omwe atha kusewera mphindi 90 komanso ena oti atha kusintha zinthu titavutika. Masewero alero timavutika mchigawo choyamba, mmene tinakonzera simmene zinalili komabe titasintha komanso kuwayankhula nthawi yopumulira, osewera anachita bwino kwabasi." Anatero Mponda.
Mmasewerowa, Binwell Katinji, Gift Chunga komanso Chinsisi Maonga ndi omwe anagoletsa zigoli za timuyi. Iwo asewera masewero atatu ndi MAFCO komanso Kamuzu Barracks kupatikizira a Bangwe ndipo apambana onse.
Mutumize pa namba iyi 0991509953
@clementina tatumiza
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores