Komiti ya ochemelela yomwe imayang'anila za umoyo wa osewela kutimu ya Silver Strikers, yathandiza osewela otchedwa Tatenda M'balaka yemwe pakadali pano ndiovulala.
Mwambo opeleka ndalamazi unachitika dzulo pabwalo la Silver pakutha pamasewelo omwe ma Banker anagonjetsa MAFCO FC 3-2.
Poyankhula atatha kupeleka thandizoli, King 'No Fear' Malaya yemwe ndi wapampando wa ochemelela komaso membala wa komitiyi, anati apeleka ndalama yomwe sanatchule kuchuluka kwake, kuti ithandize pazosowa zina za osewelayu komaso ngati chilimbikitso kwa osewela.
Iye anapitiliza kulimbikitsa ochemelela a timuyi kuti apitilize kulimbikitsa osewela a Silver Strikers ndimathandizo osiyanasiyana akakhala ovulala.
Ndalamazi zinasonkhedwa pa gulu la WhatsApp la komitiyi yomwe inasonkhetsanso masapota ena omwe anafika pa bwalo la Silver dzulo.
WOLEMBA: Erik Chiputula
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores