MWANSA WABWELERA KU MAFCO
Timu ya MAFCO yalengeza zoti mphunzitsi wawo, Prichard Mwansa wabweleraso kutimuyi ndipo atsogolera timuyi ngati mphuzitsi wamkulu mu 2024.
Mmodzi mwa akuluakulu atimuyi, Godfrey Makawano, watsimikiza kuti Mwansa wachoka ku Moyale pomwe wabwerera kuti akapitilize pomwe anasiyira chaka chatha.
Iye wati MAFCO inayamba kale zokonzekera masabata apitawo ndipo akonza kuti chaka chino atengekonso chikho chimodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores