"SITIKAFIKANSO KU MAPENATE TIKAYIMALIZIRATU" - ANONG'A
Mtsogoleri wa osewera akale a timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Fischer Kondowe, wati timu yawo ikamalizitsa zonse ikamatha mphindi 90 pomwe akukumana ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers akalekale.
Kondowe wati masewerowa ndi amtengo wapatali ndipo mavuto awo onse awakonza chomwe akufuna ndi chipambano.
"Masewero tinayamba kukonzekera kalekale ndipo tili serious ndi masewerowa. Tinali ndi vuto kumbuyo koma zonse takonza ndipo tikayimaliziratu palibe zofika mphindi 90." Anatero Kondowe.
Matimuwa akukumana ngati gawo limodzi lopeza ndalama zothandizira bungwe lomwe alikhazikitsa kuti lizithangata osewera akale a matimu awiriwa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores