"ALI NDI TINGONGOLE TATHU AKABWENZA LERO" - MSANGALA
Osewera wa timu yakale ya Mighty Mukuru Wanderers, James Sangala, wati osewera atimu ya FCB Nyasa Big Bullets yakale ali ndi ngongole zomwe abwenze pomwe matimuwa akukumana masana a lolemba pa bwalo la Kamuzu.
Sangala wayankhula patsogolo pa masewerowa pomwe wati palibenso kunyengererana pomwe akufuna akabwenzere zomwe Bullets inkawachita mmbuyomu.
"Masewero tawakonzekera ndipo mukudziwa kale ali ndi tingongole tathu tina ndi tina ndipo leroli akabwenza timeneto. Kaya anatigonjetsa kaya kutenga chikho pamwamba pathu zonsezo akalipira lerolo." Anatero Sangala.
Matimuwa akukumana kuti apeze ndalama yomwe ithandizire ntchito ya bungwe lomwe lakhazikitsidwa kuti ithangate umoyo wa osewera akale a matimuwa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores