SILVER ICHOTSA OSEWERA KHUMI
Timu ya Silver Strikers ikuyembekezeka kuchotsa osewera okwana khumi pomwe ikuyamba zokonzekera zokhwima za ligi ya chaka chino.
Mkulu wa timuyi, Patrick Chimimba, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati timuyi ikufuna ntchito za osewera omwe asewera mu timuyi kuti izichita bwino komanso kuti amadikira lipoti ya aphunzitsi atimuyi.
Osewera monga George Chaomba, Tathedwa Willard, China Chirwa ndi ena ndi omwe akumveka kuti atha kuona nsana wanjira.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores