RAMADAN ABWERA MWEZI WA MAWA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Nsanzurwimo Ramadan, sanafikebe kutimuyi ndipo akuyembekezeka kudzayamba ntchito pa 1 March 2024.
Mkulu woyendetsa ntchito zatimuyi, Tiyasomba Banda, watsimikiza zankhaniyi kunena kuti mphunzitsiyu akadali ndi timu yomwe akuphunzitsabe ku Tanzania koma achoka kumapeto a mwezi uno.
"Mphunzitsiyu anapereka kalata kuti achoka kumapeto amwezi uno komwe akugwirako nde tikumuyembekezera kuti afika pa 1 March. Sitikudandaula chifukwa ndi zimenenso tinkayembekezera nthawi yomwe tinkamupatsa ntchito." Anatero Banda.
Padakali pano, wachiwiri kwa mphunzitsiyu, Meke Mwase ndi amene akutsogolera timuyi.
Mphunzitsiyu anauzidwa kuti ayitsogolerere timuyi kutenga ligi ya TNM komanso zikho ziwiri zapadera ndipo chimodzicho atha kusiyirako ena.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores