CHITIPA YATENGA KAFOTEKA
Timu ya Chitipa United yalengeza kuti yatenga mphunzitsi watimu ya Extreme FC, Elvis Kafoteka kuti awatsogolere mu ligi ya chaka chino.
Kafoteka wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi timuyi ndipo polemba pa tsamba lake la Facebook wathokoza anthu onse ku Extreme FC kamba kokhala naye bwino.
Iye wati akuyembekezera zabwino kutimu ya Chitipa kuti ikhalanso ikuchita bwino mu ligi.
Iye walowa mmalo mwa Macdonald Mtetemera yemwe anachoka kutimuyi chaka chatha kupita ku Creck Sporting Club.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores