"NDIKUFUNA NDITAVALA MENDULO CHAKA CHOYAMBA" - KUDONTO
Wosewera yemwe wakwezedwa kupita kutimu yaikulu ku Mighty Mukuru Wanderers, Dan Kudonto, wati alibe mantha kutumikira timuyi ndipo akufunitsitsa atavala mendulo mu chaka chake choyamba.
Iye wati umoyo wake kutimuyi wayamba bwino ndipo akiyembekezera kaye kuphunzira zambiri kuchokera kwa ankhala kale kutimuyi komabe akukhulupilira kuti Wanderers situluka chimanjamanja chaka chino.
"2024 ndayikonzekera bwino kwambiri ndipo zinthu ndipanga. Mukudziwa kuti ikhala season yanga yoyamba kumenya supa ligi ndiye kuzikhalabe kuphunzira koma ikhala season yabwino matimu aatiziwa."
Kudonto amasewera pakati motchinga ndipo ndi mmodzi mwa osewera omwe akwezedwa kuchokera kutimu yachisodzera yomwe inakwanitsa kutenga zikho ziwiri chaka chatha.
Wolemba Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores