A NKUNIKA ATSOGOLERABE MASAPOTA A WANDERERS
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yatulutsa mayina a ochemerera atimuyi omwe akhale akutsogolera anzawo kwa zaka ziwiri zikubwerazi.
Mu kalata yomwe wasaina mmodzi mwa akuluakulu a board ya timuyi, Chancy Gondwe, yotulutsidwa lachinayi yati a Mervin Nkunika ndi omwe atsogolerebe ochemererawa ndipo a Bishop Chimwenje akhala owatsatira ndipo mlembi wamkulu ndi Davie Pemba komanso Chikhulupiliro Mphatso awatsatira.
Timuyi yaikanso chigawo chakummawa ngati gawo lina kuphatikiza pa kumpoto, pakati komanso kummwera.
A Mike Kamanga atsogolera chigawo chapakati, a Joseph Bolamoyo atsogolera kumpoto, a Dennis Chitsulo kummwera ndiponso a Davie Monjeza atsogolera kummawa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores