"MASAPOTA AYEMEKEZERE ZAMBIRI ZOKOMA" - KATINJI
Katswiri yemwe wasainidwa nditimu ya Silver Strikers, Binwell Katinji, wati ochemerera atimuyi ayembekezere zabwino zokhazokha pomwe wati agwira ntchito ngatinso mmene amachitira kumatimu ena.
Iye amayankhula atasaina mgwirizano wa zaka ziwiri kutimuyi kutsimikiza za kubwereranso kutimuyi ndipo wati ndi wokondwa kubwereranso kwawo.
"Ndine wosangalala poti ndabwereranso ku Silver, nditimu yoti ndasewerapo, khalidwe lake ndikulizidziwa komanso zambiri nde ndasangalala. Masapota amayembekezera zambiri koma ndi zoti sindingagwire ntchito ndekha komabe ayembekezere zabwino zambiri ngati mmene ndimachitira ku matimu ena." Anatero Katinji.
Katswiriyu wapita kutimuyi mwaulere kutsatira kutha kwa mgwirizano wake ndi Civo komwe anamwetsa zigoli 12 mu ligi ya chaka chatha.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores