DEDZA YASAINA CHIKUFENJI
Timu ya Dedza Dynamos yalengeza kuti yasaina katswiri wosewera kumbuyo kapenanso pakati watimu ya Mighty Tigers, Frank Chikufenji, yemwe wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ku Mbatatesiku.
Iye wapita kutimuyi mwaulere kutsatira kutha kwa mgwirizano wake ndipo wati wakondwa kamba kopita kutimuyi.
"Ndine wosangalala poti ndasaina ndi timu yabwino yatsogolo ngati iyi ndipo ndikuona kuchedwa kuti ndiyambe kugwira ntchito pa bwalo. Dedza yakhala timu yakumaloto kwanga angakhale tikamakumana nayo ndipo lero zatheka." Anatero Chikufenji.
Ndipo mlembi wamkulu watimuyi, Kondwani Banda, wati ichi ndi chiyambi chokunga timu yamphamvu yoti ichite bwino ndipo ikhala ikusainanso osewera ena mmasiku akubwerawa.
Timuyi inathera pa nambala yachisanu ndi chiwiri ligi cha chaka chatha ndipo iyamba zokonzekera zawo lolemba likudzali.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores