"SINDINAGANIZE KAWIRI ATANDIPEZA A SILVER" - CHIPALA
Wosewera pakati ndi kutsogolo yemwe timu ya Silver Strikers yasaina lachiwiri, Charles Chipala, wati linali khumbo lake lalikulu kuti adzasewereko timu yaikulu ngati Silver Strikers.
Iye amayankhula pomwe amamuonetsa kutimuyi kuti wasaina mgwirizano wa zaka zitatu pomwe tsopano wachoka kutimu ya Dedza Dynamos pa ndalama zomwe samaziulule.
Iye wati ndi wokondwa kupita kutimuyi ndipo akuyembekezera kuti ayithandiza timuyi kuchita bwino ndipo iye athandizika kuti apite patsogolo ndi mpira wake.
"Kubwera Ku Silver Strikers ndi chinthu chapamwamba kwambiri chifukwa ndi zimene ndakhala ndikukhumbira nthawi yaitali nde atandipeza sindinaganizirenso kawiri koma kuvomera." Anatero Chipala.
Iye wakhala osewera wachitatu kupita kutimuyi patsogolo pa ligi ya 2024 pomwe inatenga Christopher Gototo komanso Macdonald Lameck kuchokera ku Dedza Dynamos.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores