FOMO YASANKHA BWALO LA MULANJE PARK
Timu imene yangolowa kumene mu Supa ligi, FOMO, yasankha bwalo la Mulanje Park ku bungwe la Football Association of Malawi kuti ndi limene agwiritse ntchito ngati bwalo lawo lapakhomo patsogolo pa ligiyi.
Timuyi yasankha bwaloli poti iyo ndi yaku Mulanje ndipo apereka ku FAM ngati mbali imodzi yokwanilitsa zomwe timu ikuyenera kukhala nazo pa ndondomeko ya Club licensing.
Ndipo woona za ndondomekoyi, a Cassper Jangale, atsimikiza kuti tsopano ayamba kuyendera mabwalo osiyanasiyana mdziko muno kuyambira 26 February ndipo ndandanda wa mabwalo omwe avomerezedwe udzatuluka pa 13 March.
Nayo khonsolo ya mzinda wa Mulanje yati ikukonza zofunikira pa bwaloli kuti likhale pa mulingo wochititsa masewero amu ligi yaikuluyi.
Timuyi imalephera kugwiritsa ntchito bwaloli ikusewera mu ligi yaing'ono kamba ka kusamvana pakati pa iwo ndi khonsoloyi ndipo amakasewera ku bwalo la Esperanza mu mzindawu.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores