BINWELL KATINJI WAYAKA MOTO KU ZAMBIA
Katswiri waku Malawi, Binwell Katinji, akuchita bwino mdziko la Zambia komwe akuyesa mwayi pomwe wamwetsa zigoli zisanu ndi ziwiri (7) pa masewero atatu omwe wasewera ndi timu ya Mufulira Wanderers.
Katswiriyu anapita kutimuyi komwe akukayesa mwayi pomwe timuyi inaonetsa chidwi chofuna kumutenga itatha ligi ya TNM mmwezi wa December.
Iye alibe mgwirizano uliwonse ndi timu iliyonse pomwe mgwirizano wake ndi Civo unatha pa 31 December 2023.
Mu ligi ya chaka chatha, iye anagoletsa zigoli 12 za Civo pomwe anali wachinayi pa anthu omwetsa zigoli zambiri ndipo yemwe anagoletsa zigoli zambiri, Clement Nyondo, anamwetsa zigoli 16.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores