BULLETS NDI WANDERERS AKUMANA PA 04 MARCH
Matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Mighty Mukuru Wanderers akuyembekezeka kukumana koyamba chaka chino pa 4 March 2024 pamwambo omwe osewera akale amatimuwa akufuna kutolera ndalama zothandizira bungwe la osewera akalewa.
Izi zadziwika ku Lali Lubani kunyumba ya Wanderers komwe bungwe la osewera akale amatimuwa lakhazikitsidwa ndipo asankha Kelvin Moyo kukhala mtsogoleri wa bungweli.
Moyo wati iwo alingalira zokhazikitsa bungweli kamba ka imfa ya osewera wakale wa Wanderers, Jack Chamangwana, ndipo sakufunanso kuti osewerawa azivutika.
Masewero pakati pa matimuwa ndi ofuna kupeza ndalama ya bungweli ndipo Yasin Osman adzaphunzitsa Wanderers pomwe Kinnah Phiri adzatsogolera FCB Nyasa Big Bullets.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores