"NDIMACHITA BWINO CHIFUKWA CHA PASUWA" - MWAUNGULU
Katswiri yemwe wasewera bwino kuposa aliyense mu Supa ligi ya 2023, Patrick Mwaungulu, wati kuchita bwino kwa iyeyo ndi chifukwa choti Callisto Pasuwa amamuthandiza.
Iye anayankhula atapambana mphotoyi lachisanu ku Mount Soche ku Blantyre ndipo wati Pasuwa ndi yemwe wamuthandizira kwambiri.
"Ndikuthokoza Mulungu kamba koti ndapambana chaka chino, chaka chatha anangondisankha koma sinnapambane komabe apapa ndapambana. Ndithokoze osewera anzanga komanso mphunzitsi wathu Pasuwa poti amandikhulupilira, ndikakhala sinnasewere bwino amandipatsabe chilimbikitso." Anatero Mwaungulu.
Katswiriyu anaithandiza kwambiri Bullets kuti ipambane chikhochi kachitatu kolumikiza ndipo anagonjetsa Chimwemwe Idana, Innocent Nyasulu ndi Clement Nyondo pa mphotoyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores