GABA NDI ANZAKE ANYANYALA MASEWERO
Timu ya Moroka Swallows yomwe mumasewera katswiri waku Malawi, Gabadinho Mhango, ikuyembekezeka kutaya mapointsi okwana asanu ndi imodzi pomwe osewera atimuyi anyanyala kamba kosapatsidwa ndalama zawo.
Malipoti ochokera ku South Africa atsimikiza kuti timuyi sisewera Mamelodi Sundowns madzulo a lero komanso Golden Arrows yomwe amayenera kukumana nayo mmasiku akubwerawa.
Osewera onse atimuyi kuphatikizapo Mhango anakana kupanga zokonzekera dzulo komanso kuchita m'bindikiro pokonzekera masewerowa kamba koti akufuna ndalama zawo atapatsidwa ndi akuluakulu atimuyi.
Zateremu ndekuti Mamelodi Sundowns yatola mapointsi apatebulo kwa lero ndipotu Arrows ikuyembekezeka kuchitanso chimodzimodzi mu masiku akudzawa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores