"TIMAONA NGATI SIZITHEKA KOMA ZATHEKA" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wathokoza anyamata ake kamba kochilimika mpaka kupambana pomwe wati amaona ngati nzovuta kuti angatero.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe Chimwemwe Idana anagoletsa pa mphindi 95 kuti Silver Strikers igonjetse Kamuzu Barracks 2-1 mu ligi ndipo wayamikira anyamata ake.
"Analidi masewero ovuta koma tinasewera bwino makamaka mchigawo choyamba pomwe tinatsogola pa chilichonse koma kachibwana mchigawo chachiwiri kanatibweretsa mmbuyo komabe pomwe zimaoneka ngati sizitheka, zatheka." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver Strikers yafika pa nambala yachiwiri mu ligi ndi mapointsi 56 kutsatira chipambanochi ndipo izipempherera kuti Karonga United igonjetse FCB Nyasa Big Bullets kuti iwo idzagonjetse Bullets yokha mmasewero omaliza.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores