"NDI ZOKHUMUDWITSA NDIPO SIZINGAPITITSE MPIRA PATSGOLO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wati ndi wokhumudwa kamba koti ochemerera atimu yawo anagendedwa ndikuvulazidwa ndi ochemerera atimu ya Silver Strikers ndipo wati sizoyenerera mu mpira.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa Silver 1-0 ndipo anati ndi wokondwa ndi mmene anyamata anasewerera pa bwalo la zamasewero koma zoti ena anagendedwa ndi zokhumudwitsa.
"Anyamata asewera bwino, mchigawo choyamba mwina timakanika kusewera bwino timamenya mpira wammwamba koma mchigawo chachiwiri tinasintha ndipo tinayamba kupanikiza mpaka kupeza chigoli, tasewera ngati timu lero tiwayamikire anyamata koma ena agendedwa zomwe zili zokhumudwitsa." Anatero Chirwa.
Chipambano cha timuyi chaitengera pa mapointsi 29 pomwe yafika pa nambala 8 ndipo wasewera masewero 21. Bungwe la Super league of Malawi silinayankhulepo za chipolowechi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores