"ZIVUTE ZITANI MAWA TIKUSWA EXTREME" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati timu yake yakonzekera kuti apeze chipambano mmasewero awo ndi Extreme FC pomwe akufuna kuchoka ku chigwa cha matimu otuluka mu ligi ya TNM.
Iye wayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe alipo pa bwalo la Nankhaka ndipo wati mavuto omwe anali nawo okanika kugoletsa zigoli awakonza ndipo akonzeka kutchisa Fodya waku Mchinji.
"Takonza mmene timakonzekerera masewero aliwonse koma awawa tipita ndi cholinga kwambiri chifukwa sizikutiyendera mu ligi. Chomwe chimativuta ndi kupeza zigoli nde ndi zimene taunikirapo kwambiri ndipo anyamata tawauza kuti mwa njira iliyonse tikapambane. Extreme nayo ilinso kumunsi nde sibwera mwachibwana komabe tiyesetsa kuti tipambane." Anatero Chingoka.
Awa akhala masewero oyamba ngati mphunzitsi watimuyi a Chingoka ndipo ngati angapambane, iwo atuluka mu munsi kwa ligiyi. Moyale ili ndi mapointsi 23 pa nambala 14.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores