"TIKUYENERA KUWINA MWA NJIRA ILIYONSE" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati timu yake inayiwala kale zakugonja kwawo ndi timu ya Chitipa United ndipo wati akuyenera kupambana mwa njira iliyonse ndi timu ya Red Lions.
Mkandawire wayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe alipo pa bwalo la Balaka ndipo wati akukhulupilira kuti akhala ovuta potengera kuti Red Lions ikumenyera nkhondo yoti itsale mu ligi koma iwo akufuna chipambano.
"Anyamata akonzeka ndipo chimene tikuyang'ana ndi kuti titapambana masewero amenewa omwe atifikitse pa mapointsi 31 omwe tikuyang'ana ndithu. Mu sabata yonseyi takhala tikukonza kumbali yomwetsa zigoli ndipo anyamata akagwira ntchito." Anatero Mkandawire.
Timu ya Bangwe ili pa nambala 7 mu ligi ya TNM pomwe yatolera mapointsi 28 pa masewero 21 omwe asewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores