"DEDZA NDI TIMU YABWINO" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati akukhulupilira kuti masewero awo ndi timu ya Dedza Dynamos pa bwalo la Champions ku Dowa akhala ovuta kamba koti timuyi ndi yabwinonso.
M'gangira wayankhula izi pomwe amayankhula ndi olemba nkhani patsogolo pa masewerowa ndipo wati akukasewera pa bwalo loti sanasewerepo koma akukhulupilira kuti akapambana.
"Ndi masewero ovuta poti Dedza ndi timu yabwino, sungangopita kuti ukatenga mapointsi utangokhala, ukufunika kulimbikira nde tikupita mmasewerowa titapambana ndi Moyale zomwe zikupereka molalo kwa osewera komanso kuti anagoletsa ndi osewera atatu osiyanasiyana, zikupereka chithunzi kuti aliyense atha kugoletsa." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver ikapambana masewerowa, ifika pamwamba pa ligiyi pomwe padakali pano ali ndi mapointsi 36 pa nambala yachinayi mmasewero 20.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores