NYONDO SAPEZEKA NDI SILVER
Timu ya Dedza Dynamos itha kukhalabe yovutika kupeza zigoli pomwe katswiri wawo, Clement Nyondo, sapezeka mmasewero awo ndi timu ya Silver Strikers kamba kovulala.
Mphunzitsi watimuyi, Gilbert Chirwa, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati Nyondo wangoyamba majowajowa koma sangapezeke mmasewerowa chimodzimodzi Limbani Phiri yemwenso ndi ovulala. Iye wati Joseph Balakasi ndiyemwe wachira koma wati masewero ndi Silver ndi ovuta.
"Sikoyamba kukumana nawo ndipo si zachilendo kukumana nawo komano tikudziwa kuti ali ndi timu yabwino, osewera abwino anagonjetsa Moyale ndi zigoli zambiri koma ife ngati Dedza tipita olimba mu mphamvu ndi mzeru." Anatero Chirwa.
Dedza Dynamos ili pa nambala yachikhumi pomwe ili ndi mapointsi 26 pamasewero makumi awiri (20) omwe yasewera. Ngati ali ovulala, Nyondo akutsogolabe ndi zigoli mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores