"OYIMBIRA ANATIBALALITSA NDE TAGONJA" - MHANGO
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Nicolas Mhango, wati oyimbira anasokoneza timu yake kuti igonje ndi timu ya Silver Strikers pomwe wati zigoli zoyamba za Silver sizinali zoyenera kukhala zigoli.
Mhango amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonja 4-1 pa bwalo la Bingu ndipo timu yake ndi imene inayamba kugoletsa koma Silver inamwetsa zinayi. Iye wati oyimbira anawabalalitsa osewera ake.
"Timu yanga inayamba bwino koma anakhumudwa ndi mmene oyimbira anachitira, chigoli choyamba sichinali penate ndipo chachiwiri sichimayenera kukhalanso chigoli nde zinawafoola osewerawa." Anatero Mhango.
Iye anati anayesetsa kuwauza osewera awo kuti achilimike kuti asewerebe ndikupeza mwayi otsalabe mu ligi pomwe ali pa nambala 14 ndi mapointsi 23 pa masewero 21.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores