"ZA UKATSWIRI ZITAYENI IFE TIKUYANG'ANA CHITSOGOLO" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati zoyankhula zokhudza ukatswiri wa chikho cha TNM zisakambidwe kaye pomwe timu yake ikuyang'ana kuti kutsogolo kwao kukhala motani.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Moyale Barracks 4-1 pa bwalo la Bingu kuti abwenzere maganizo ofuna kulimbirana ukatswiri wa ligiyi. Iye wayamikira anyamata ake kamba kopeza chipambanochi.
"Ndife osangalala ndi chipambanochi, tinachinyitsa mwachangu koma anyamata anaazipereka ndipo anachilimika mwachangu, ndi zokondweretsa kuti tapeza chipambano chachikulu pakhomonso. Za kutenga ligi zitayeni kaye ife tikuyang'ana kutsogolo kuti tione masewero oti tipambane." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver Strikers ikadali pa nambala yachinayi pomwe tsopano ili ndi mapointsi 36 pa masewero 20 omwe asewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores